Mwandidodometsa Anasibeko

NTHANO
MWANDIDODOMETSA A NASIBEKO
WOLEMBA: INNOCENT MASINA NKHONYO
Ndinakoka mpando wawutali pa malopo nkudziponya mosangalala. Ndinali ndi chifukwa chokwanira chomwetulilira panthawiyo. Ndimkadziwa kuti wa masese wofululidwa mwa chingoni utsopedwa patsikulo.
“Amayi tathirani zisanu ziwiri zibwelere” Zoonadi kachetechete sawutsa nyama koma suyosuyo, anayimba wezuro Kwalirakape amene ife timkangoti Kwalira pomunyadira. Ukutu kunali kuyambitsa mwambo wopambanawo. Ndi Kwalirayutu amene amkakanyamula chakumwacho ife tili peche pa mpando mitu yathu ya panke titadendekera ngati atonkhwetonkhwe. Samawilingula Kwalira. Akanatani munthu woti analibe ngakhala khobili logulira ndudu ya chingambwe. Kunyamula mapaketi achakumwacho inali mbali yokhayo imene Kwalira akanatenga pa gulu la matchona a kutawuni ngati ife.
Tinayamba kutsinkha molapitsa mowawo kwinaku chingerezi chopanda malamulo ndi nthabwala zikulikitimuka kukometsa mwambo wa chingoniwo. Nawo wodziwa kutakasa ziwuno anali chapoteropo kuthobotsa miyendo m’mwamba, thukuta likuchucha ngati mtsinje wa Bua. Nawo anachiwona chanzeru kudzakometsa mwambowo.
“Koma mudzi wathuwu amaupezelera ndithu” Anayifinya nkhani a Mbiyazapolama amene anakhala moyang’anana nane pa mwambo wopha chikokeyaniwo.
“Zitheka bwanji kuti nduna za gogo Chalo zichite kukwana zisanu zochokera mmudzi mwa mfumuyi chonsecho mudzi wathuwu palibe wapatsidwa unduna? ” Anakhuthura maganinzo ake onse Mbiyazapolama kwinaku maso ali pa mtunda ngati wameza ng’oma ya nyau ija amati mbalule. Zinalidi zopweteka kuti gogo Chalowo anasankha nduna zokwana zisanu kuchokera m’mudzi mwake chosecho m’midzi ina yozungulira panalibe ndi mmodzi yemwe anasankhidwa unduna. Ngakhale ndimamva kuwawa ndi mchitidwe wokonderawu sindinathyolepo mnkhwani pa nkhaniyo. Pajatu ndinali nditangofika kumene kumudziko kuchokera ku tawuni kumene ndinakatchona.
“Tabwerani apa a chimwene tilawe nawo timve kuti mthupimu zikhala bwanji.” Uyu anali mayi wina amene anakhala pagulu la amayi azake kuyitana njonda yina imene imangochita zunguliruzunguliru pamolopo ndi thumba la mizu, zoperapera ndi timaphukusi tambwibwi zodziwa yekha. Ndimkaganizabe za kupezeka kwa amayiwo pa mowapo. Kenaka ndinakumbukira zimene anandiwuza Ndengundengu kuti pa Chingoni amayi nawo amadzipereka pa mwambo wolemekeza chakumwawo. Kenaka ndinawona amayi aja akulawa zimene njondayo imagulitsa mseko uli pakamwa.
“Ndilawe nawo amwene.” Uyu anali mnyamata amene anakhala pafupi ndi pamene pamachitikira malonda amphakapo.
“Choka! Uli ndi nkhali iwe kapena ufuna ukangotaya? ” Anakalipa mayi amene amawoneka wachikulirepo pagululo. Nditasinkhasinkha tanthaunzo la nkhali, ndinaumvera chinsoni mtundu wanga. Ndinazindikira chimene njonda yopanda manyaziyo imagulitsa. Kodi dzikoli likupita kuti? Ndinadzifunsa funso limene linandikanika kuyankha.
Pa nthawi yonse imene ndinakhala pamalopo ndimadabwa ndi mkabwalo mwina momwe amkapititsamo osati mapaketi a mowa koma ndowa za mowa. Ndinatchera khutu kuti ndimve zimene mabwana amayitanitsa ndowawo amakambirana.
“Ukawerenge buku la Yohane ndime sindikuwuza, amati Yesu anasandutsa madzi kukhala vinyo. Ndiye ife ndife yani kuti tikanyoze chozwizwitsa choyamba cha mwana wa Mulungu? ” Ndinazindikira kuti amalankhulayo anali katswiri pa malembo woyera.
“Ifetu timangokumwa sitimaphunzitsa ana uthakati” Anathilira ndemanga wina. Nditafufuza bwino za madolo anzeruwo, ndinazindikira kuti anali akuluakulu akumpingo kwathu kudzatenga nawo mbali mobisalira pa mwambo wolemekezekawo. Ndinakhumudwa zinali zachidwiwikire kuti anthu a Mulunguwo amamwera chopereka chathu chimene tinapereka sabata imeneyo.
Kadzuwa kanayamba kuonetsa zizindikiro zotsazikana nafe. Nthawi ina iliyonse mdima watsokomola nngakusumbe chipumi ukanatikumbatira ndi mapiko ake. Ngakhale zinali choncho sitinayiwale malonjezo athu pa malopo woti tiwupapira mowa molapitsa mikoko yogona.
“Tikamaliza uwu tithire mkaka mowa umene ubwerewo.” Ndinapereka maganizo amene ndimayembekezera kuti asangalalatsa aliyense. Mmalo moti Kwalirakape ndi Mbiyazapolama akondwe ndi maganizowa ndi Mbiyazapolama yekha anaonetsa nkhope ya chimwemwe.
“Ine mundipatsa padera mowawo chifukwa sindikufuna kumwa mkaka mukunenawo pajatu enafe za miyendo inayizi sitimadya.” Uyutu anali Kwalirakape kutiuza zakukhosi. Tinayang’anizana ndi Mbiyazapolama modabwa ndi zimene ananena Kwalirakape. Ndinakanika kupilira ndipo ndinalivumbulutsa funso.
“Ndiye mkaka tikunenawo uli ndi miyendo inayi? ”
Mmalo mondiyankha funsolo mwachilungamo anandiponyera lake funso Kwalira.
“Kodi mkaka mukunenawo ndiwankhuku ya miyendo iwiri kapena wa ng’ombe ya miyendo inayi? ”
Sindinamuyankhe. Panalibe chifukwa choti ndizilimbana naye Kwalirakape pa nkhani ya mkaka ndichiwerengero cha miyendo ya ng’ombe.
Chikhumbokhumbo chokayimilira chinandipeza. Sindinachedwe kudikira kuti ndinyowetse buluku, ndinavumbuluka pamalopo. Chifukwa choledzera mopsola mulingo ndinapunthwa ndisanafike pa malo woyenera kutaya madzi. Chifukwa choti sindimkafuna kulikitimuka ngati chikuni chowuma, ndinadzilimbitsa ndi khoma limene linali pafupi. Mwatsoka ndinadziponya mwamphabvu kukhomako ndipo linagwera mkati. Linali losalimba chifukwa choti linali lasungwi. Dothi limene limaoneka ngati zidina pa chikupapo linali longomata.
Zimene ndinaona mkatimo khomalo litagumuka zinandidodometsa. Ndinaona a Nasibeko, mayi amene amatigulitsa mowa pa malopo, akuzunguliza mtsikana wina ndi mthiko wotakasira mowa. Chinandidodometsa kwambiri ndi mtsikanayo. Ngakhale ndinaledzera mowonjezepo nkhope ya mtsikanayo siyikanandisowa. Anali Malifa, mtsikana wa mayi Nasibeko amene anamwalira mosadziwika bwino chaka chatha. Manja ake anali woduka komanso analibe mapazi. Ndinanjenjemera ndipo theka la mowa umene ndinapapira pa tsikulo unasungunuka. Nzeru nazo zinandithera. Ndiye kuti zimene amanena anthu zoti a Nasibeko anakhwimira Malifa kuti mowa uziwayendera zinali zoona eti? Ndinadzifunsa funso limene silimasowekera yankho.
“Achimwene mwangoti chilili apa mukutani? Tachokani msanga! Kuledzera mopusaku mwandilaula nako.” Analitu a Nasibeko kulira ngati mwana wa khanda atangondiona.
“Aah..aaa…kungoti.. ndimafuna kutaya madzi.” Ndinayankha koma modziluma lilime.
“Ndiye kutaya madziko mpakana kugumula khoma? Tachokani apa musandinyanse! ! ! ”
Zifukwa zochokera pa malopo zinali zitakwana kale nthawi yomwe ija ndinaona Malifa, malemu Malifa. Sindimasowekeranso kudikira mayiwa kundiuza chochita. Sindinakodzenso mwaulemu monga mwa chikozero changa. Panthawiyi nkuti mkodzo utanyowetsa kale buluku langa.
“Kodi ambwana sindinamve zoti Malifa anamwalira? ” linalitu funso limene ndinaliponya kwa Mbiyazapolama nditangofika pamene timamwera mowa paja.
“Eyatu anamwalira msungwana uja, mzimu wake wuuse mumtendere. Nanga bulukuli lanyowa ndi chiyani? Kuzolowera kumwa thobwa eti? ”
Mmalo moyankha kapena kupereka ndemanga pa mafunso achipongwewo, ndinangowauza azangawo kuti tichokepo pa malopo. Sindinalabadire za mowa umene tinali titagula kale ndinawauza azangawo kuti tichokepo basi. Ineyo ndimkadziwa kuti ndine mwana wa mngoni ndipo sindimandenguka ndi mowa mwachisawawa. Zoti ndinakodzedwa chifukwa choti ndinazolowera thobwa anali maganizo chabe a Mbiyazapolama. Akanakhala kuti Mbiyazapolamayo anaona zimene ndinaona ine sindikukayika, akanachita zina zoposera kukodzedwa kumene ndinakodzedwa ineko.

by Innocent Masina Nkhonyo

Other poems of NKHONYO (60)

Comments (0)

There is no comment submitted by members.