(26 March 1920/22 - 25 July 2002 / Magura / Bangladesh)

Amalawi Tikuponderezedwa Ndi Alendo

ZAKUKHOSI/MAGANIZO ANGA

AMALAWI TIKUPONDELEZEDWA NDI ALENDO


WOLEMBA: INNOCENT MASINA NKHONYO

Mtundu wina uliwonse wa anthu umadziwika ndi zimene mtunduwo umakonda kuchita; zabwino ndi zoipa zomwe. Nchifukwa chaketu sizodabwitsa kumva ndemanga zoti anthu akutiakuti aja ndiwokonda nkhondo kapena mtundu wakutiwakuti uja ndiwolimbikira ntchito. Tithokoze Mulungu kuti mtundu wathu wa Amalawi timadziwika ndikulandira alendo bwino chimene ndi chinthu chonyaditsa kwambiri. Ndifedi achikondi kwa anthu wobwera ndipo nzosakayikitsa kuti mu Afrika muno tili patsogolo pa nkhani ya mkomnya kwa alendo.

Chifukwa cha kudekha kwathu komanso chikondi chathu chosefukira kwa alendo, zikukonetsa kuti ena mwa anthu wongobwera atengerapo mwayi womatipezerela, kumatidyera masuku pa mutu pa nkhani ya malonda. Kwa amene mumakhala ku madera ngati Chinsapo, Mchesi, Ndirande ndi Madera ena wofananilanapo ndi amenewa mzichitochito, mungathe kundiyikira umboni kuti penapake anthu wobweradi ngati Maburundi akutiphangira mwayi wochita malonda ang’onoang’ono amene tikanamachita ife Amalawi, eni nthaka. Kunena mwatchutchutchu sindikudziwa kwenikweni chimene likuchita bungwe lija lowona za anthu olowa ndi kutuluka mdziko muno pa zifukwa zosiyanasiyana pa nkhaniyi. M’maganizo anga ndili ndi chikhulupiliro kuti pali malamulo amene abale athu wongobwera m’dziko muno ayenera kutsatira. Ngati malamulowodi alipo ndipo ngati bungwe ndikunenali limagwiritsadi ntchito malamulowo ndiye sindinganenenso mobisa kuti malamulowo ndiophweka kwambiri kuyerekeza ndi mayiko ambiri pa dziko lapansili. Tikati tiwonetsetse Amalawi anzathu amene ali m’mayiko ena amayenda ali chewuchewu kuwopa kufunsidwa mafunso awiri atatu. Tikanena zakuno, ngakhale mBurundi angathe kukutulutsira mawu achipongwe mopanda mantha. Funso nkumakhala lakuti ifeyo tachita kutani chikondicho kuchifikitsa pamenepa. Kunena mosalumpha Chinyanja chikondi chathu kwa anthu obwera nchopanda tanthauzo kwenikweni ngati sitilabadira tsogolo la a Malawi azathu, eni dziko.

Momwe ndikuonera ine palibe nzeru kumangoyang’anira anthu wobwera, ngakhale wothawa nkhondo akumachoka m’malo momwe akuyenera kukhala nkumadzatilanda mwayi wochita malonda m’mizindamu. Ena angathe kunena kuti wopusa ndi ifeyo Amalawi chifukwa malonda amatikanika tokha pamene anzathuwa monga Maburundi amachita bwino pa msika. Chabwino awo ndi maganinzo enanso koma m’maganizo angawa sindikuona kuti ndife opusa poti alendo akutichitira bwino m’dziko lathu lomwe. Pali zifukwa zambiri zimene ife sitikuzidziwa zimene Maburundi ndi anthu ena obwera amachitira bwino pa msika. Nkhani yayikulu ndiyakuti boma kudzera ku unduna wowona za anthu wolowa ndi kutuluka m’dziko muno lichitepo kanthu pa nkhaniyi.

Ife monga anthu wokonda mtendere sitifuna kuti zinthu zidzafike mpakana za ku Joni zija ayi. Koma tikamangowonelera alendowa akutikhomelera chonchi idzafika nthawi imene Amalawi adzayimike manja m’mwamba kuti talephera kupilira kupezeka mwachisawawa kwa alendo m’dziko muno. Ichotu chidzakhala chipwirikiti choopsa ngati cha ku Joni chija. Pozindikira kuti mumvi woyang’anira suchedwa kulowa m’maso ndikuona kuti nthawi yakwana yoti bungwe ndi unduna umene ukukhudzidwa ndi nkhaniyi achitepo kanthu. Alendo onse afufuzidwe. Akapezeka ena kumalo kumene sakuyenera kupezeka abwezeredwe msanga kumalo kowayenera. Chikonditu amanena kuti chimayambira kunyumba chisanasefukire kwinaku. Nanga ngati amvula zakale sananame pozukuta mwambiwu, tilolera bwanji kuti m’Malawi mnzathu wa malonda azigulitsa paketi imodzi ya shuga pa tsiku chonsecho mlendo akugulitsa mazanamazana a mapaketi a shuga?

M’mbuyomu a Polisi amathamangitsa anzathu wobwerawa kumadera ndatchula aja koma sipamatenga nthawi yayitali kuti abwelere. Zikuonetsa kuti akuluakulu ena; mafumu ndi mabwana a bungwe lina lake; komanso apolisi ena akumalandirako kangachepe kuchokera kwa alendowa ndikumawabisa m’madera amene sakuyenera kupezeka. Akuluakulu amene akuchita izi akuyenera kudziwa kuti akuzuzitsa Amalawi wosauka amene amapeza zosowa pa moyo wawo pochita malonda wosiyanasiyana m’madera momwe Maburundi amangamo maziko. Akuluakulu adyerawa asadzadabwe tsiku lina akadzaona Amalawi wosauka ndikunenawa akugwiritsa ntchito njira zina zosayenera kuthana ndi vutoli. Zidzakhala zochitititsa manyazi kwa Mmalawi wina aliyense wokonda mtendere. M’maganizowa sindikufuna kuwuza Amalawi kuti ayambe kutola miyala kukagenda magolosale a Maburundi. Ngati Amalawi wokonda mtendere, aliyense ali ndi udindo wosunga chithuzithuzi chathu chabwinochi. Koma ngati chinachake sichichitika pa nkhaniyi, ndithu tsiku lina mtsogolo muno miyala idzatoledwadi kukachita nayo zosayenera pa malonda a Maburundi ndi alendo ena wosatsata malamulo.

User Rating: 5 / 5 ( 0 votes )

Other poems of NKHONYO (60)

Comments (0)

There is no comment submitted by members.