Zoonadi Titukule Amayi Koma........

ZAKUKHOSI

ZOONADI TITUKIRE AMAYI KOMA………

WOLEMBA: INNOCENT MASINA NKHONYO

Mphini yobwereza ndiimene imawala anatero amvula zakale. Nzosadabwitsatu tsono kumva nkhani ina yake ikubwerezedwa kawirikawiri. Tikatsekula mawayilesi sitikumalephera kumva nkhani imeneyi. Kwa iwo amene ali ndi mwayi wopezako manyuzipepala pa nkhani zimene akumawerenga sipakumalephera nkhani yoti titukule amayi. Apatsidwe mwayi amayi wofanana ndi wa amuna, ukumaterotu uthengawo. Ngati sindikunama pali chingerezi chake chimene chikumakulumunyidwa amayiwa akafuna kugwira ntchito zimene m’mbuyome amagwira abambo okha.

Kunena mosakondera maganizo otukula amayi powapatsa maudindo wofanana ndi amuna ndi maganizo anzeru ndithu. Ngakhale tsiku ndi tsiku tikuyamikira maganizowa kuti afika pa nthawi yake, nzomvetsa chinsoni kuti nkhani yokweza amayi penapake tikuyitengera pa mgong’o. kwa amayi amene analeledwa mwa chimalawi ndi moopa Mphambe Chiothamisi, angathe kundiyikira umboni kuti amayi ena atengerapo mwayi pa mfundo zotukula amayi kuti ayambe kuzuza abambo. Mmaganizo angawa sindikufuna kuthetsa nkhondo yomenyera ufulu wa amayi ayi komano nkhondoyo tiyeni tiyimenye modekha. Tisapsinje nayo abambo chifukwa kumeneko nkulakwiranso abambowo. Panopa mmene anthu akuwumvera ufulu wa amayi kukubweraku tisadzadabwe kuona abambo akuchita zioenetsero nawonso kumenyera ufulu wa abambo.

Pamene tikumenya nkhondo yokweza amayi tikuyenera kumvetsa kuti ntchitoyi siyatsiku limodzi. Mfundo zoti amayi ndi abambo asamasalane pa ntchito ndizochokera ku mayiko a kuulaya, kwawo kwa azungu ndipo tikanena kuti tizikhazikitsa tsiku limodzi kwathu kuno ndiye tingonamapo. Zotsatira zake zofuna kukhala ngati tili ku mangalande, kufuna kuphunzira zonse za azungu tsiku limodzi ndi zimene zikumathetsa mabanjazi.

Ena angathe kuganiza kuti ndine wa chimidzi kwambiri chifukwa ndikukakamirabe za chikhalidwe cha chimalawi chomaona ntchito zina zake ngati za amuna okha. Chabwino ndikhale ndi chimidzi changacho koma ngati ndinu bwana pa kampani ina yake mumuyiye mzimayi pa mpando wina wake chifukwa choti myeyo ndi mzimayi kusiya amuna amaphuziro wokwanira. Mupange zimenezi kwa chaka muone ngati simugwetsa kampaniyo. Pa mfundo imeneyi sindikufuna kunena kuti abambo onse ndiwophunzira kapena wozindikira kuposa amayi onse ayi. Chimene ndikufuna kunena ndi chakuti mwayi wa ntchito, kaya wa masukulu kapena wa maudindo uperekedwe kwa aliyense mofanana kutengera ndi zowayenereza wosati chifukwa choti ndi mwamuna kapena mkazi. Tikamangopereka mwayi wa sukulu, wa ntchito, kapena maudindo kwa amayi potengera kuti ndi amayi chonsecho sakukwanira pa sukulupo, pa ntchitopo kapena pa udindopo, tisadzadabwe tikadzaona kuti zinthu sizikutiyendera bwino mdziko muno.

Pa nkhani ya mwayi wasukulu ndiye zikunyanya. Zikuonetsa kuti akazi ndiye zikuwayendera kwambiri kumbali imeneyi. Kwa amene simukudziwa choona pamenepa kapena amene mukukayikira mufufuze chiwerengero cha atsikana amene akumatengedwa masiku ano kukaphunzira msukulu za ukachenjede za boma. Muone magiredi awo ndipo muyerekeze ndi magiredi ndi chiwerengero cha anyamata, mutsimikiza kuti amuna akukumana nazo kuti apeze mwayi wopitiriza maphunziro kuyerekeza ndi amayi. Panopa akuti akufuna theka lachiwerengero cha wosankhidwawo lizikhala la atsikana ndipo theka linalo lizikhala la anyamata. Popanga izi akuyiwala kuti polemba mayeso chiwerengero cha anyamata chimakhala chachikulu tikayerekeza ndi cha atsikana.

Momwe ndikuonera pa nkhaniyi ndi bwino kuti tonse ngati Amalawi tigwirane manja kutukula dzikoli posayang’anira kuti wina ndi wamkazi kapena wamwamuna. Chimene tikusowekera ndi mtima wodzichepetsa. Kunena mosakuluwika mawu pali zinthu zina zimene amuna sangakwanitse kuchita, avomereze amunawo kuti sangakwanitsedi. Chimodzimodzi amayi, pali ntchito zina zimene amadziwa ndithu kuti ngakhale kamba atadukula kapena dzuwa litatulukira ku mzambwe sangakwanitsebe kuchita akuyenera kuvomereza zakulephera kwawo pa mbali imeneyo.

Mwachidule aliyense apatsidwe ntchito imene angakwanitse wosati chifukwa choti ndi wammuna kapena ndi wamkazi tikatero tidzamanga Malawi wabwino wachitukuko komanso wolemekeza chikhalidwe chathu. Pakutero tidzaopadi Chisumphi polemekeza chikozero chake choti mwamuna ndi mkazi akhale wosiyana ndithu m’njira zina.

by Innocent Masina Nkhonyo

Comments (0)

There is no comment submitted by members.